Mmodzi wa akuluakulu ku timu ya Mighty Wanderers ati ndiye amatsogolera anthu omwe agwidwa akuba ndalama zomwe anthu amapereka kuti aonere masewero awo ndi Sable Farming Loweluka.
Malingana ndi kafukufuku wa apolisi anthuwa ati amauzidwa zoyenera kuchita ndi mkulu wa Wanderers-yu.
Padakali pano oganizilidwa-wa atchula anthu ena awiri omwe akukhudzidwa ndi nkhaniyi omwe amangidwa.
Apolisi akupitilira ndi kafukufuku wawo kufuna kupeza mkulu yemwe amatsogolera izi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores