"SITISUNGILA OSEWERA ALIYENSE" - MGANGIRA
Mphunzitsi watimu ya Silver Strikers FC, Peter Mgangira wati sasungila osewera aliyense pamasewero omwe timu yake isewere ndi Creck Sporting Club..
Silver Strikers isewera ndi Creck Sporting Club muligi ya TNM mawa Lachiwiri pabwalo la Silver mumzinda wa Lilongwe.
Masewerowa akudza pomwe timuyi ikhale ikunyamuka kulowera m'dziko la Tanzania kumasewero achibwereza nditimu ya Young Africans kumathero a sabata lino.
Koma polankhula pa msonkhano wa olemba nkhani Lolemba, Mgangira wati awalangiza osewera a timuyi kuti sakuyenera kutengeka ndi zotsatira za mumpikisano wa CAF Champions League ndipo m'malo mwake akuyenera kulimbikira kuti apeze chipambano.
Mwazina, Mgangira wati alibe chonamizira chilichonse pamasewerowa kaamba koti osewera ake ambiri amene anali ovulala tsopano achila ndipo akhala akupanga zokonzekera nditimuyi.
"Creck Sporting Club nditimu yabwino kwambiri koma nthawi zonse ndimanena kuti timapereka ulemu kutimu iliyonse
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores