Timu ya dziko lino ya Flames yachoka pa nambala 126 kufika pa nambala 128 kutsatira kusachita bwino kwa timuyi pa masewero omwe ankakumana ndi timu ya Sao Tome and Principe mu mpikisano wopitira ku chikho cha World Cup.
Malawi yatsika pa ndandanda wa dziko lonseli kamba koti inagonja ndi timu yomwe ili pansi pa iwo kwambiri zomwe zikuonetsa kuti anatayanso ma points ochuluka kwambiri.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores