Timu ya MAFCO yachenjeza anthu omwe akufalitsa zoti goloboyi wawo, Christopher Mikuwa, analandira ndalama kuti apereke zigoli zophweka ku timu ya Mighty Wanderers kuti akuwafufuza ndipo alandira zomwe akuzisaka kamba koyipitsa mbiri ya osewerayu.
Mu kalata yomwe timuyi yatulutsa yatsutsa mphekeserazi ndipo yati goloboyiyu sanachiteko kanthu kokayikitsa kuti amatenga ndalama kuti azipereketsa zigoli ku matimu ena.
Iwo ati sanamuyimitsekonso Mikuwa kuti asagwirire mmasewero awo a mtsogolo ngati monga malipotiwa akukambira.
MAFCO inagonja 1-0 ndi Wanderers pa chigoli chimene anagoletsa Blessings Mwalilino pa mphindi 51 za masewerowo pa bwalo la Champions ku Dowa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores