MAFCO yadandaula ndi oyimbira atagonja ndi Wanderers
Mphunzitsi watimu ya MAFCO FC, Stereo Gondwe, wati oyimbira pa masewero awo ndi Mighty Wanderers anawabalalitsa mchigawo kuyithandiza Wanderers kuti ipambane mmasewerowa.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-1 kuti atuluke mu chikho cha FDH Bank ndipo wati panalibe vuto lililonse kuchokera ku timu yawo kuti agonje koma oyimbira basi.
"Anyamata asewera bwino kwambiri maka mchigawo choyamba Koma mchigawo chachiwiri oyimbira anatisokoneza kwambiri basi tiwayamikire a Wanderers kuti apambana ife tibwerera tikapange za ligi." Anatero Gondwe.
Timuyi tsopano iyika chidwi chawo mu ligi pomwe adzakumane ndi timu yomweyi ya Mighty Wanderers sabata ya mawa pa bwalo la Champions ku Dowa pakuyamba kwa chigawo chachiwiri cha ligi.
Chithunzi : CEE JAY Photography
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores