Nkhani
Timu ya Bangwe All Stars yatsimikiza kuti mtsogoleri wa osewera, Fanizo Mwansambo, wachoka kutimuyi ndipo wapita ku Mighty Wanderers pa mtengo womwe sanaunene.
Timuyi yalengeza za nkhaniyi kudzera pa tsamba lawo la Facebook ndipo lamufunira zabwino zonse pa ulendo wake.
Komabe ngakhale zili chomwechi, mmodzi mwa akuluakulu ku timu ya Bangwe wati Mwansambo anasaina kale ndi timu ya Ekhaya FC mgwirizano wa zaka zitatu.
Iye wati katswiriyu amafuna kuthetsa mgwirizano ndi Bangwe kamba koti panadutsa miyezi itatu asakulandira ndalama komabe zinali zisanatheke komabe anasaina ku Ekhaya.
Ngati nkhaniyi ili yoona ndekuti Ekhaya inasaina kale Mwansambo koma inasaina osewera yemwe ali ndi timu kale timu yake isakudziwa omwe ndi mlandu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores