"KU MALAWI KULI LUSO KUPOSA KU USA" - KADUYA
Wosewera wakale watimu ya Silver Strikers, Adiel Kaduya, yemwe tsopano akusewera mdziko la United States of America wati akutha kusiyanitsa mpira wa mdziko muno ndi kwa azunguku kuti kuno kuli osewera a luso ochuluka.
Kaduya yemwe amasewera timu ya Masters Athletics yomwe ndi ya sukulu ya ukachenjede ya Masters mu dzikoli amayankhula atafika mdziko la Mozambique pomwe akukatumikira mu timu ya Malawi U-20 ku mpikisano wa COSAFA.
Iye wati a Malawi atalimbikira kwambiri ndi masewero ampira atha kupita nawo patali poti komwe aliko anthu amangosewera mwa chimenyemenye kusiyana ndi kuno.
Poyankhula patsogolo pa mpikisanowu iye anati: "Ndine wokondwa poti dziko langa linandikumbukira ndipo osewera anzanga ndi aphunzitsi andilandira bwino, ndiyesetsa kuti ndigwire ntchito yomwe ndabwerera, chomwe Mulungu wakonza ndi chomwecho."
Masewero oyamba atimuyi aliko lachisanu nthawi ya 3 koloko masana pomwe akukumana ndi dziko la South Africa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores