SAVIELI, KUDONTO, MAPEMBA NDI ENA AWATULUTSA KU FLAMES U-20
Osewera okwana asanu omwe akupanga nawo zokonzekera za timu ya Malawi Under 20 atulutsidwa mu m'bindikiro wa timuyi pomwe akuwaona kuti iwo anadutsa zaka 20.
Osewera wa Mufulira Wanderers ku Zambia, Emmanuel Savieli, awiri a Mighty Mukuru Wanderers Dan Kudonto komanso goloboyi Vincent Ganizani, wa FCB Nyasa Big Bullets Crispin Mapemba ndi yaing'ono yawo Andrew Lameck ndi omwe tsache lawapeza.
Mkulu woyang'anira chitukuko cha masewero ku bungweli, Benjamin Kumwenda, wati akuunikirabe mwa osewera ena omwe ali ku timuyi ndi cholinga choti ayende ndi osewera okhawo omwe ali ndi zaka zoyenera popita ku mpikisano wa COSAFA.
Malawi ikatenga nawo mbali mu mpikisano wa COSAFA Cup womwenso ndi wopitira ku AFCON pomwe ali mu gulu C pamodzi ndi South Africa, Comoros komanso Lesotho ku Mozambique ndipo mpikisanowu udzayamba pa 26 September 2024.
Source: Times
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores