"TINGOLEMEKEZA MAGANIZO A MABEDI KOMA AZIWINA" - KAMAU
Mmodzi mwa anthu oyankhulapo pa nkhani za masewero mdziko muno, Kim Kamau, wati mphunzitsi watimu ya dziko lino akuyenera kuyesetsa kuti aziwina poti akulandira ndalama zochuluka Kwambiri kusiyana ndi aphunzitsi amdziko muno omwe anagwirapo ntchitoyi.
Kamau amayankhula kutsatira kugonja kwa timuyi 2-3 ndi timu ya Burundi pa bwalo la Bingu ku Lilongwe ndipo wati kusiyidwa kwa osewera ena ngati Precious Sambani kukuonetsa kuti pena mitu ya aphunzitsi sikugwira ntchito.
"Iwowo amadandaula kuti alibe wotseka kumbuyo kumanzere yemwe mutimumo analipo kale kukhala Sambani nde paulendowu kumusiya kusonyeza kuti mutuwu abalalika pang'ono. Burundi ndi timu yocheperako mphamvu ndi Burkina Faso ndipo titha kukavutikako kumeneku komabe tingolemekeza maganizo a mphunzitsiyu." Anatero Kamau.
Iye anati anthu amafunikira kupeza chipambano ndi chifukwa chake akumakuwa kuti Mabedi achoke ndipo ngati mmodzi mwa aphunzitsi omwe akulandira ndalama z
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores