SAMBANI WASIYIDWA KU FLAMES
Mphunzitsi watimu ya Malawi, Patrick Mabedi, wasiya osewera yekha yemwe anali otseka kumbuyo kutimu yake, Precious Sambani, paulendo wake wopita ku Burkina Faso.
Izi zikudza pomwe Mabedi anadandaula kuti osewera akumbali imeneyi akuvuta kwambiri ndipo anamenyetsa Gomegzani Chirwa yemwe anavutika kwambiri ndikupezeka mu kulakwitsa mu zigoli ziwiri pa masewero omwe Flames inagonja 3-2 ndi Burundi.
Atatha masewerowa, Mabedi anati anamenyetsa Chirwa kumbaliyi kamba koti anakwanitsapo kuchita bwino ku African Cup of Nations mu 2022.
Osewera ena omwe asiyidwa ndi Charles Chisale wa Extreme FC, Maxwell Paipi, Chikondi Kamanga, Uchizi Vunga a Silver Strikers, Nickson Nyasulu ndi Wongani Lungu a FCB Nyasa Big Bullets komanso Gaddie Chirwa wa Mighty Mukuru Wanderers.
Timu ya Malawi ili ndi masewerowa lachiwiri mdziko la Mali komwe akukakumana ndi Burkina Faso mmasewero achiwiri amu gulu lopitira ku African Cup of Nations.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores