"NDABWERA KUDZAGWIRA NTCHITO" - CHESTER
Katswiri watimu ya Flames, Yamikani Chester, wati ndi wokondwa kamba koti wabwereranso kutimuyi pomwe wati wabwera kuti adzagwire ntchito osati kudzasewera basi.
Iye amayankhula lachitatu patsogolo pa masewero atimuyi omwe aliko lachinayi pa bwalo la Bingu ku Lilongwe ndipo wati ntchito ya dziko imafunikiranso osewera ena kuti agwirenso ntchito yomwe iwe umagwira.
"Ndine osangalala poti ndabweranso ndikhonza kunena kuti mpira ndi nthawi ndi zimafunikiranso kuti ena akagwira ntchito yomwe iwe umagwira koma apa ndabweranso, sikuti ndabwera kudzasewera koma kudzagwira ntchito kuti tithandize dziko lathu." Anatero Chester.
Iye wapempha anthu osapotera timuyi omwe ndi amalawi kuti asawachotseretu kuti mwina sachita bwino koma apite pabwalo la Bingu kuti akasapotere mwamphamvu timuyi.
Chester wakhala akusiyidwa ndi mphunzitsi, Patrick Mabedi mmbuyomu ati ponens kuti iye akukula koma tsopano waganiza zomutenga poti osewera ena amalo ngati omwewa nd
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores