"KUCHEPA KWA NTHAWI KUSAKHALE PONAMIZIRA" - BANDA
Mtsogoleri wa timu ya dziko lino ya Flames, Christopher John Banda, wati akudziwa kuti nthawi ya zokonzekera kutimuyi ndi yochepa kwambiri koma pasakhale ponamira poti osewera amapanga kale zokonzekeranso mmatimu awo.
Iye amayankhula lachitatu patsogolo pa masewero atimuyi lachinayi ndi timu ya Burundi ndipo wati osewera onse akudziwa kufunikira koyamba bwino pa masewero amenewa.
"Tikufunitsitsa titayamba bwino chifukwa osewera aliyense akudziwa kufunikira kopita ku mpikisano wa AFCON zomwe ndi zotheka ngati tizipambana masewero nde kuti ulendo ukhale wabwino tikufunika kuti tiyambe bwino." Anatero Banda.
Katswiriyu wati iwo ngati osewera alimbikira kwambiri kuti achite bwino mmasewero awo amu gulu lopitira ku AFCON ndi cholinga choti adzafike nawo ku ndime yotsiriza ya mpikisanowu.
Timuyi ikuyembekezeka kupitanso mdziko la Burkina Faso akamaliza kusewera ndi timu ya Burundi mu masewero ena amugululi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores