FLAMES IBINDIKIRA MASIKU ASANU NDI LIMODZI
Timu ya Flames ikuyembekezeka kuchita m'bindikiro kwa masiku asanu ndi limodzi (6) okha basi pomwe akukonzekera kusewera mpikisano wa masewero opitira ku African Cup of Nations.
Malingana ndi bungwe la Football Association of Malawi, timuyi idzalowa mu m'bindikirowu pa 31 August pomwe matimu onse a pansi pa FIFA adzakhale akupuma kaye kuti asewere masewero a zikho za mayiko.
Wachiwiri kwa mtsogoleri wa bungweli, Madalitso Kuyera anati iwo sakufuna kusokoneza mipikisano ya mdziko muno pomwe Flames ikusewera.
"Tikufuna m'bindikiro usamakhale kunja kwa ndondomeko ya FIFA cholinga tisamasokoneze mipikisano ya mdziko muno." Anatero Kuyera.
Izi tsopano zikudza pomwe mphunzitsi wa dziko lino, Patrick Mabedi wakhala akudandaula kuti kukonzekera kwa timuyi kukumakhala Kwa nthawi yochepa komanso kuti osewera ambiri a mdziko munomu si akupsa kwambiri zomwe zikumavutitsa kuchita bwino.
Malawi idzasewera ndi Burundi pa 5 September 2024 ndipo idzapita
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores