MKONDA WAPITA KU ZAMBIA
Katswiri yemwe wathetsa mgwirizano wake kutimu ya Mighty Mukuru Wanderers, Francis Mkonda, ali mdziko la Zambia komwe akukayesa mwayi kutimu ya Kabwe Warriors ya mdzikomo.
Izi zadziwika malingana ndi mmodzi mwa olemba nkhani mdziko muno, Twaha Chimuka, yemwe wati wapeza kuti osewerayu watuluka kale mdziko muno.
Katswiriyu akhala wachisanu ndi chimodzi ngati anasaine mgwirizano ndi timuyi pa osewera a mdziko muno omwe akusewera mdziko la Zambia komwe kuli Robert Saizi, Chawanangwa Kaonga, Christopher Kumwembe, Emmanuel Savieli ndi Chifundo Mphasi.
Iye anathetsa mgwirizano wake ku Wanderers kamba koti nthawi yosewera imachepa ndipo anati afotokoza bwino za tsogolo lake.
Source: Twaha Silva Chimuka
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores