"TIWONJEZERA OSEWERA ATATU" - MWALWENI
Mphunzitsi watimu ya Baka City, Kondwani Mwalweni, wati timu yake iwonjezera osewera atatu pomwe msika wogula ndi kugulitsa osewera watsegulidwa kuti akweze ndikukonza Malo omwe akuwavuta.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-0 ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Karonga ndipotu wati wavomereza kugonja kwawo koma akukanika kugoletsa mpake abweretse osewera ena.
"Mukakhala kuti mwaphonya mipata chilango chake chimakhala chimenechi, tinaphonya mpata wabwino mchigawo choyamba koma tinaphonya nde tagonja tivomereze." Anatero Mwalweni.
Iye wati osewera omwe abwerewo ndi wakutsogolo ndi apakati chifukwa ndi malo amene timuyi ikuvutika makamaka mchigawo choyamba cha ligiyi.
Timuyi yathera pa nambala yomaliza yeniyeni mu ligi itatha chigawo choyamba pomwe ali ndi mapointsi asanu ndi awiri (7) pa masewero 15.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores