"TIKUFUNA KUPAMBANA NDI WANDERERS" - KAUNDA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Oscar Kaunda, wati timu yawo yakonzekera kuti apeze chipambano pamwamba pa timu ya Mighty Mukuru Wanderers pomwe akukumana nayo loweruka.
Iye wayankhula patsogolo pa masewerowa omwe aseweredwe pa bwalo la Kamuzu ndipo wati akuwatenga masewerowa ngati aliwonse poti chipambano chimafanana kwa matimu onse.
"Tikadakonzekerabe masewerowa poti tikufunika kuti tipeze chipambano pa masewerowa loweruka. Tikukonzekera monga masewero aliwonse poti kupambana ndi Wanderers ndi mapointsi atatu, kupambana ndi Creck ndi mapointsi atatunso nde tachita chimodzimodzi basi." Anatero Kaunda.
Timu ya Karonga United ili pa nambala yachisanu ndi chiwiri (7) pomwe ili ndi mapointsi asanu ndi atatu (8) pa masewero asanu omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores