"TIKUFUNA KUKHALA OYAMBA KUPHA SILVER" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati wakambirana ndi osewera ake kuti timu yawo ikhale yoyamba kugonjetsa timu ya Silver Strikers kumathero kwa sabatayi.
Mtetemera wayankhula patsogolo pa masewerowa omwe akukumana lamulungu pa bwalo la Silver ndipo Mtetemera wati ngakhale anyamata awo ena sapezeka kamba koti ali pa ngongole kuchokera ku Silver Strikers, timu yake ichita bwino.
"Takonzekera bwino kwambiri tikufuna kuti sitikhala ndi osewera ena chifukwa anachokera pangongole ku Silver komweko koma tili ndi anyamata oti atha kugwira ntchito ndipo ifeyo tawauza anyamatawa kuti tikhale oyamba kugonjetsa Silver ndipo ndi zotheka chifukwa nafe 3 points tikuyifuna." Anatero Mtetemera.
Anyamata omwe sapezeka ndi Akuzike Lifa, Emmance Nyirenda komanso Tathedwa Willard kamba ka migwirizano kuti sadzisewera akakumana ndi Silver komanso George Chaomba ali ndi kadi yofiira.
Creck Sporting Club ili pa nambala 9 po
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores