"POINT IMODZI SIZINAYIPE" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati kupeza point imodzi pa masewero awo si zinthu zolakwika pomwe wati masewero tsopano ayamba kuvuta mu ligi.
Mwansa amayankhula atafanana mphamvu ndi timu ya Dedza Dynamos ku Mzuzu ndipo wati timu yake ndi yabwino ndipo yangotsala kukonza zinthu zochepa.
"Anali masewero abwino mwina tinasewera bwino mchigawo choyamba pomwe tinapeza mipata ingapo koma sitinathe kugonjetsa pomwe mchigawo chachiwiri anzathu anabwera komabe sitinachinyitse nde kupeza point imodzi sizinaipe poti tsopano mpira wavuta ndipo matimu ayamba kuchita bwino." Anatero Mwansa.
Timu ya Moyale ili pa nambala 6 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi 7 pa masewero anayi omwe asewera. Iwo apambana kawiri, kufanana mphamvu kamodzi ndi kugonjanso kamodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores