"OYIMBIRA SANAGWIRE BWINO NTCHITO" - BUNYA
Mphunzitsi watimu ya Dedza Dynamos, Andrew Bunya, wati kupatula kuphonya mipata yawo, oyimbira sanagwire bwino ntchito yake zomwe zachititsa kuti asapeze chigoli.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 ndi Moyale Barracks ndipo wati sakudziwa kuti kunali kukondera kapena kusadziwa ntchito koma oyimbira wakanika kugwira ntchito yake.
"Tinakonza kuti mchigawo choyamba tiwasunge koma mchigawo chachiwiri tipite kutsogolo kwambiri nde koma mipata tinayipeza tinaphonya koma ina timagwetsedwa mu box koma oyimbira sanafune kuyimba, osati kuti timafuna kukonderedwa koma ntchito yawavuta." Anatero Bunya.
Timu ya Dedza Dynamos ili pa nambala 13 mu ligi pomwe ili ndi mapointsi atatu pomwe yafanana mphamvu katatu ndi kugonja kamodzi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores