"TASANGALALA KWAMBIRI NDI MMENE ZATHERA" - SEMU
Wothandizira kwa mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Joseph Semu, wati zomwe anawauza osewera atimuyi zinayenda pomwe anati akangotseka kumbuyo kuti Wanderers isapeze mpata.
Iye amayankhula atatha masewero omwe anafanana mphamvu 0-0 ndi Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Mpira ku Blantyre ndipo anati ndi wokondwa ndi zotsatirazi.
"Anali masewero abwino ndipo tithokoze kuti osewera achita zomwe tinawauza kuti Wanderers ndi timu yaikulu ndipo ndiyovuta maseweredwe awo nde tikangotseka kumbuyo kwathu ndipo ndine wokondwa ndi zotsatirazi." Anatero Semu.
Timuyi tsopano yatsitsa kufika pa nambala 15 pomwe yakwanitsa kufanana mphamvu kawiri ndi kugonjanso kawiri kuti akhale ndi mapointsi awiri pa masewero anayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores