"NTCHITO ILIPO KOMA TIPANGE ZA WANDERERS KAYE" - MSUKWA
Mphunzitsi wogwirizira watimu ya Bangwe All Stars, Mapopa Msukwa, wati timuyi ili ndi zambiri zofunika kukonza komabe angoonetsetsa kuti achite bwino ndi Wanderers.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Mpira lamulungu ndipo wati kuphunzitsa timu imene simachita kale bwino sikumapereka phuma lililonse.
"Zokonzekera zikuyenda bwino kuti mwina tichite bwino mmasewerowa, zoti tikonze nde ndi zochuluka komabe tikungofuna tionetsetse kuti tigwire zokhudza masewero akubwerawa kenako tiyambe kukonza bwinobwino. Palibe phuma lililonse, timu yachonchi ikagonja sangati vuto ndi iwe koma tiyesetsa kukonza kuti izichita bwino." Anatero Msukwa.
Mphunzitsiyu wayipeza timuyi ili pa nambala 16 mu ligi pomwe yatolera point imodzi pa masewero atatu omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores