"TIKUFUNITSITSA KUCHITANSO BWINO" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati timu yake ikufunitsitsa kupeza chipambano loweruka kuti iyiwale za kugonja kwawo ndi timu ya Mighty Mukuru Wanderers sabata yatha.
Nginde amanena izi lachisanu patsogolo pa masewero awo ndi Mzuzu City Hammers ndipo wati akonza mavuto awo onse kuti mwina achite bwino mmasewerowa.
"Tikuchoka kogonja komwe tinangopereka ndipo zinatipweteka koma tsopano takonzeka kuti tichite bwino, zonse zovuta takonza mwina poti Hammers ndi timu yabwino koma takonzekera kuti tipambane basi." Anatero Mtetemera.
Iye watinso timu yake ikumagoletsetsa zigoli kwambiri ndipo mavuto amenewa akonzedwa ndipo ndi Hammers achita bwino.
Creck ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) ndi mapointsi asanu ndi imodzi (6) pa masewero atatu omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores