"TIKUMAMVETSETSA ANYAMATA POTI NDI ATSOPANO" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati anyamata ake akonzeka kwambiri kuti achite bwino pomwe akukumana ndi timu ya Chitipa United pakhomo pa bwalo la Mulanje Park lamulungu.
Iye amayankhula patsogolo pa masewerowa ndipo wati timu yake ikumasewera bwino mmasewero omwe agonjako koma akumawamvetsetsa pakuti ndi atsopano mu ligi ya TNM.
"Masewero omwe takhala tikusewera timachita bwino koma mwina zolakwika zing'onozing'ono ndi zimene zimatipweteketsa koma tikumawakonzabe poti ndi atsopano tikumawamvetsetsa." Anatero Chirwa.
Iye watinso timu ya Chitipa ndi yabwino koma khumbo lawo ndi loti masewero apakhomo azikwanitsa kuchita bwino.
Timu ya FOMO ili pa nambala 12 pomwe yatolera mapointsi atatu pa masewero atatunso omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores