LIGI YA CHIPIKU IZILANGA OSABWERA PA BWALO
Bungwe loyendetsa mpira mchigawo chapakati la Central Region Football Association lati likhale likupereka zilango kwa matimu omwe akhale asakupita mmabwalo kukasewera masewero omwe apatsidwa mu ligi ya chaka chino.
Mlembi wamkulu wa bungweli, Antonio Manda, wanena izi pa mkumano waukulu wa bungweli kumathero a sabata yatha ndipo wati achita izi poti matimu ambiri anachita mchitidwewu chaka chatha.
"Ndichenjeze matimu onse kuti imene izikhala osapita pa bwalo izilipira ndalama ku CRFA yokwana K500,000 ndipo akachita zimenezi Kwa masewero otsogozana atatu, izichotsedwa mu ligi pompopompo." Anatero Manda.
Ligiyi iyambe pa 28 April 2023 lomwe ndi loweruka likudzali ndipo mwambo wokhazikitsa chikhochi uchitika pa bwalo la Dowa pa boma komwe timu ya Dzaleka Future idzakumane ndi Blue Eagles.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores