"OMWE ANATISANGALATSA SABATA YATHA NDI OMWEWA" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Abbas Makawa, wati akhale akuwalimbikitsa osewera ake kuti ayambirenso kuchita bwino poti ndi osewera ake omwewa omwe anapambananso sabata yatha.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi Moyale Barracks pa bwalo la Mzuzu lero ndipo wati akonze monse molakwika kuti mmasewero ena azachitenso bwino.
"Lero zativuta tagonja kwambiri koma mwina tikanatha kupamba mu chigawo choyamba chomwe taphonya kwambiri koma zimachitika tiwalimbikitsa anyamatawa poti ndi omwewa omwe anatikondweretsa sabata yatha nde tiyesetsa." Anatero Makawa.
Timu ya Civo yayamba motsimphina mu ligi ya chaka chino pomwe yapambana masewero amodzi ndi kugonja awiri ndipo ali pa nambala yachisanu ndi chitatu (8).
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores