"TIKUFUNA TISAMATAYE MA POINTSI PAKHOMO" - MWANSA
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati ndi wokondwa kamba koti timu yake yapeza chipambano chawo chachiwiri mu ligi ya TNM ya chaka chino ndipo wati akufuna kuti azichita bwino masewero apakhomo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 3-0 ndi timu ya Civo United ndipo wati salekera pomwepa pomwe alimbikitse osewera ake kuti azichita bwino.
"Tasewera bwino kwambiri ndipo tapambana masewerowa anyamata anachita bwino ndipo timafunitsitsa kupambana uku poti timachoka kogonja nde zakhala bwino poti tikufunitsitsa kuti masewero apakhomo tizichita bwino kuti kwa Ife tikhale tilibwino." Anatero Mwansa.
Timu ya Moyale tsopano yafika pa nambala yachitatu mu ligi pomwe ili ndi mapointsi asanu ndi imodzi (6) pa masewero atatu omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores