"TIKAKHAZIKIKA TIZIPAMBANA MASEWERO" - CHIRWA
Mphunzitsi watimu ya FOMO FC, Gilbert Chirwa, wati timu yake imangopanga zibwana zing'onozing'ono zomwe zachititsa kuti agonje masewero omwe amakumana ndi Kamuzu Barracks.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-1 pa bwalo la Champions ndipo wati tsopano akapeza luntha losewerasewera mu ligiyi ndikukhazikika ayamba kuchita bwino.
"Zoonadi timangochita tizibwana mpake anzathu amachinya zigoli nde ndi zodandaulitsa koma tikuyenera tiphunzire kuti muligi mulibe chisoni nde Poti nkoyamba ambiriwa kusewera ligiyi tikuphunzira ndipo tikakhazikika posachedwapa tiyamba kupeza zipambano tsopano." Anatero Chirwa.
Timu ya FOMO tsopano yagonja kawiri motsatizana ndipo inakwanitsa kupeza chipambano mmasewero oyamba ndipo ili pa nambala yachikhumi ndi mapointsi atatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores