"WANDERERS YASEWERA BWINO KWAMBIRI" - MTETEMERA
Mphunzitsi watimu ya Creck Sporting Club, Macdonald Mtetemera, wati timu yake sinasewere bwino ndipo wavomereza kugonja Kwa timuyi koma wati sikutha kwawo.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 3-0 ndi Mighty Mukuru Wanderers pa bwalo la Kamuzu ndipo wati akonza mavuto awo kuti apitilize kuchita bwino.
"Lero tavutika kwambiri, sitinasewere mmene timasewerera ndipo Wanderers yasewera bwino tiwayamikire, athu ndi mavuto aang'ono oti tikabwerera tikakonza. Sikuti tagwa ayi koma mwina zindilimbikitsa kuti ndikonze mavuto ens ndi ena kupita chitsogolo." Anatero Mtetemera.
Timuyi tsopano yatsika kufika pa nambala yachisanu pomwe ikadali ndi ma pointsi asanu ndi imodzi (6) pa masewero atatu omwe asewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores