"MAPENATE AWIRI TIKANAPATSIDWA" - GONDWE
Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Stereo Gondwe, wati timu yake ikanatha kupatsidwa mapenate awiri mmasewero omwe amasewera ndi Baka City koma oyimbira anaona mosiyana.
Gondwe amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 ndi Baka City ku Karonga ndipo wati kusakhals bwino kwa bwaloli komanso ziganizo za zoimbira zina zakanikitsa kuti apambane.
"Anali masewero abwino kwambiri mwina tinasewera bwino koma bwaloli madzi ndi kuterera zinatikanikitsa kuti mwina tisewere mpira wathu koma kuchoka ku Salima kudzatenga point imodzi ndi zabwinonso. Mwina tikanatha kupeza mapenate awiri osewera wathu anagwetsedwa koma oyimbira anayimba kona tingovomera kuti ndi mmene anaonera." Anatero Chirwa.
Zateremu, MAFCO ili pa nambala 12 mi ligi pomwe yakwanitsa kutenga ma points awiri pa masewero atatu omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores