"TSOPANO TIYAMBA KUWINA" - MUYOMBE
Mphunzitsi watimu ya Baka City, Davie Muyombe, wati tsopano timu yake ikuphunzira pang'onong'ono ligi ya TNM ndipo mmasewero otsatira ikhale ikupeza chipambano chawo choyamba.
Iye amayankhula atatha masewero omwe afanana mphamvu 0-0 ndi MAFCO ndipo wati mipata yomwe anaphonya mchigawo choyamba ndi yomwe akanatha kupambanira.
"Tinasewera bwino koma taphonya mmipata ya mchigawo choyamba mwina tikanatha kutsogola 2-0 koma mchigawo chachiwiri sitinali bwino timamenya mpira wa mmwamba komabe tikuphunzira apa tapeza point imodzi ndekuti masewero otsatira tipeza chipambano poti Ife tikuchokera ku Simama nde tikuphunzira ndithu." Anatero Muyombe.
Timu ya Baka City tsopano yapeza point yawo yoyamba mu ligiyi pomwe tsopano yasuntha kufika pa nambala 13 ndi point imodzi pa masewero atatu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores