"TIKUFUNIKA KUTI ALIYENSE AZIGOLETSA" - MAKAWA
Mphunzitsi watimu ya Civo United, Abbas Makawa, wati akulimbikitsa osewera ake onse kuti azikwanitsa kupeza zigoli ndi cholinga choti asamataye mipata yochuluka kuti azipambana masewero.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero awo ndi Moyale Barracks kumathero a sabatayi pa bwalo la Mzuzu ndipo wati timu yake ikufunikira kukagoletsa zigoli zambiri kuti akapambane.
"Akhale masewero ovuta kutengera kuti tonse tili ndi ma pointsi atatu komanso kuti iwo ali pakwawo komabe takonzeka. Tikufunitsitsa kukapeza zigoli zambiri poti mumapambana ngati mukugoletsa nde titakagoletsa zambiri anzathu nkupeza mwina chimodzi ndekuti tikachita bwino nde tikufuna aliyense azitha kupeza zigoli ndekuti Civo ikondwa." Anatero Makawa.
Timuyi ili pa nambala yachisanu pomwe ili ndi mapointsi atatu pa masewero awiri ndipo masewero athawa inagonjetsa Dedza Dynamos 3-0.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores