"TILENGEZA WOTHANDIZA LIGI YA DIVISION 1 LOWERUKA" - HUMBA
Wampando wa bungwe loyendetsa mpira kummwera, Raphael Humba, wati loweruka akhale akulengeza Kampani yomwe izithandiza ligi yaing'ono ya bungweli kwa chaka chino.
Humba anayankhula motere pomwe amatsimikiza kuti ligi yaikulu yakummwera iyamba lowerukali ndipo wati tsiku lomweli ndi lomwe aonetse kampaniyo.
"Chaka chino SRFA yabwera mwa mkokomo ndipo anthu aonanso kuti tabwera ndi moto apa loweruka tikhale tikuonetsa wothandiza ligi ya Division One chifukwa tinayamba kukamba za zimenezo kalekale nde lowerukali tibwere nayo nkhani yonse." Anatero Humba.
Ligiyi imathandizidwa ndi a Football Association of Malawi chaka chatha ndipo tsopano bungweli lapezano kampani yoti ithandize.
Matimu a Red Lions komanso Ntaja United ndi omwe atsegulire ligi yaikulu yakummwerayi pomwe padzakhalenso mwambo woonetsa kampaniyi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores