"OYIMBIRA AYAMBA BWINO KWABASI" - KALICHERO
Mlembi wa bungwe la oyimbira mdziko muno, Chris Kalichero, wayamikira oyimbira a mdziko muno kuti ayamba bwino pomwe agwira ntchito yapamwamba mu sabata yoyamba ya ligi.
Kalichero wayankhula izi ngakhale kuti aphunzitsi ena adandaulapo ndi mmene oyimbira anachitira koma iye wati sangalephere anthu ena ongodandaula zabodza.
"Tithokoze oyimbira onse kuti achita bwino kwambiri ndipo ayamba bwino mwina asunga zomwe tinawauza kuti zomwe aphunzira azigwiritse ntchito. Pa anthu onse opita ku masewero sipangalepheredi odandaula koma onse tawaonera, palibe walakwitsapo." Anatero Kalichero.
Mu chaka chatha, matimu ochuluka anadandaula ndi kayimbilidwe ndiponso zipolowe zimayamba kamba mchitidwewu. Mphunzitsi watimu ya MAFCO, Stereo Gondwe komanso Callisto Pasuwa wa Bullets anadandaulako za oyimbirawa mu sabata yoyamba yomweyi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores