"TINACHULUTSA KUWADERERA A FOMO" - NYAMBOSE
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Christopher Nyambose, wati timu yake yagonja kamba koti osewera ake amadelera timu ya FOMO ndipo anataya mimwayi yochuluka.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-0 pa bwalo la Mulanje ndipo wati ngakhale zili chomwechi, timu yake inachitabe bwino mu mbali zina.
"Anali masewero abwino koma sanali abwino Kwa iye poti tagonja, ndi zowawa kubwera kuno kenako nkudzagonja komabe tinawadelera anzathuwa mpaka zativuta koma tikonza mavuto athu tikonza." Anatero Nyambose.
Hassan Luwembe anagoletsa chigoli cha FOMO pa mphindi 77 za masewerowa kuti Bangwe igonje. Timuyi ili pa nambala 15 kutsatira kugonja Kwa masewerowa.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores