BANGWE YANYAMUKA KUPITA KU MOZAMBIQUE
Timu ya Bangwe All Stars yanyamuka kupita mdziko la Mozambique komwe akukasewera ndi timu ya UD Songo ku masewero apaubale omwe achitike loweruka.
Mwini wake watimuyi yemwenso ndi mtsogoleri, Mphatso Jika, watsimikiza za ulendowu pomwe wati upindulira kwakukulu timuyi pomwe akhala akuyamba ligi ya chaka chino.
"Tikupitadi ku Mozambique ndipo anatilembera kalata masabata awiri apitawo ndipo sitinachitenge chophweka ayi kutengera kutinso ndi timu yaikulu. Sindikudziwa kuti mwina Mark Harrison pomwe ali ku Malawi timamupatsa masewero otani koma ndekuti ngakhale timagonja koma amaona kaluso kenakake mwa ife." Anatero Jika.
Ndipo poyankhulapo, mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Christopher Nyambose, wati masewerowa amuthandiza kupeza timu yeniyeni yoti agwiritse ntchito mu ligi ya TNM.
"Awawa ndi masewero amphamvu poti tikumenya ndi timu yaikulu yoti mu Africa muno amayiwerengera nde zindipatsa mpata woyesa mmene tiziyambira mu ligi. Ku Betika
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores