LEO MPULULA AKUYAMBA NTCHITO MWEZI UNO
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wakawaka Tigers watsopano, Leo Mpulula, akuyembekezeka kuyamba ntchito kutimuku sabata ikudzayi pomwe timuyi ikuyamba zokonzekera mmwezi omwe uno.
Izi zikudza malingana ndi kulengeza kwa timuyi kuti ayamba zokonzekera za ligi ya chaka cha 2024 lolemba Pa 29 January pa bwalo la Mpira ku Chiwembe mu mzinda wa Blantyre.
Nthawi timuyi ikhala ikuyesanso osewera ena atsopano omwe ngati angachite bwino akasewerenso mutimuyi mu 2024.
Mpulula walowa mmalo mwa Christopher Nyambose yemwe anachotsedwa ndi timuyi kamba kosachita bwino pomwe anathera pa nambala 11 mu 2023.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores