GONDWE WACHOTSEDWA KU TIGERS
Katswiri wotseka kumbuyo ku Mighty Wakawaka Tigers, Sandress Gondwe, wachotsedwa ku timuyi pomwe mphunzitsi watsopano, Leo Mpulula, wamuuza kuti sali mu dongosolo lake.
Katswiriyu wauza Owinna kuti akuluakulu atimuyi anamufikira ndipo amuchotsa dzina lake mu kaundula watimuyi kusonyeza kuti ali ndi mwayi wosewera timu iliyonse.
"Ndi zoona, anandipeza akuluakulu ndipo andichotsa kuti ndikhonza kupita kulikonse. Ndi zowawa chifukwa sindinayembekezere komabe ndachilandira panopa ndadekha kaye kuti ndiwone komwe nditalowere." Anatero Gondwe.
Katswiriyu ali ndi tsoka pa Mpulula pomwenso mphunzitsiyu sanakondwere ndi ntchito zakenso ali ku Silver Strikers Reserve. Iye wati atiuza komwe alowere.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores