"NDAKONDWA POTI TAPAMBANA KOYAMBA KU WEST AFRICA" - MABEDI
Mphunzitsi watimu ya Flames, Patrick Mabedi, wati ndi wosangalala ndi chipambano cha timu yake ndipo wayamikira osewera kamba kosewera ndi mmene anawauzira kuti mpaka agonjetse Liberia 1-0.
Mabedi amayankhula atatha masewerowa ndipo wati zovuta zinalipo zambiri mmasewerowa komabe anyamata anayesetsa mpaka aphwanya mbiri yosapambana ku maiko akumadzulo kwa Africa.
"Mmene timabwera kuno tinapanga plan molingana ndi nyengo yakuno kuti ndi yotentha kwambiri. Mchigawo choyamba anyamata amachitako timantha pomwe samapatsirana koma titawayankhula zinasintha. Mchigawo chachiwiri kunali mvula komabe tinawauza kuti asasunge mpira kumbuyo poti umatha kuima nde liwiro la osewera latithandiza kuti tipambane." Anatero Mabedi.
Timuyi ikumana ndi Tunisia lachiwiri likudzali pa bwalo la Bingu pa masewero enanso amu gulu H lomwe Malawi tsopano ili pa nambala yachitatu pa matimu asanu ndi imodzi.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores