MKANDAWIRE WAKAYA MOTO KU ZAMBIA
Katswiri waku Malawi wosewera mpira wamiyendo koma ali mzimayi, Mercy Vitumbiko Mkandawire, wayaka moto ku Zambia pomwe dzulo wagoletsa zigoli ziwiri ndi kuthandizira zigoli zina ziwiri pomwe ZISD FC yagonjetsa National Assembly 4-1 mu FAZ National Women's Football League ku Zambia.
Katswiriyu tsopano ali ndi zigoli zisanu mu ligiyi pomwe ndi wachiwiri mu ndandanda wa atsikana omwetsa zigoli ndipo akutsogola pa ndandanda wa atsikana othandizira zigoli pomwe wathandizira zisanu chaka chino.
By Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores