"TIMAFUNA MAPOINTSI 7 KOMA ZAVUTA" - KAJAWA
Mphunzitsi watimu ya Karonga United, Trevor Kajawa, wati timu yake inayika mulingo kuti ipeze mapointsi okwana asanu ndi awiri (7) pa masewero awo atatu omwe asewera koyenda koma poti zavuta, afuna kuti abwerere ndi anayi.
Iye amayankhula izi lachiwiri patsogolo pa masewero awo ndi Dedza Dynamos ku Dedza ndipo wati masewerowa akhala ovuta poti ali koyenda komanso Dedza ifuna kuzitolera pa kugonja kwawo ndi Bullets koma akufunabe chipambano.
"Tinapanga target kuti tidzatenge mapointsi 7 koma sizinatero pano tatenga imodzi ndipo atsala atatu a mawa, tiyesetsa kuti tiwatenge amenewo kuti tibwerere ndi anayi. Akhala masewero ovuta kwambiri, Dedza tunayichinya mchigawo choyamba koma awa ndi masewero ena komabe anyamata akonzeka." Anatero Kajawa.
Timu ya Karonga ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi 32 pa masewero 23 omwe yasewera mu ligiyi.
#Tawonga2023
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores