"TIKANGOGWIRANA CHILICHONSE CHIYENDA BWINO" - AKIDU
Mmodzi mwa aphunzitsi ogwirizira kutimu ya Ekhaya FC, Fundi Akidu, wati akukhulupilira kuti timuyi ikangogwirana iyamba kupeza chipambano pomwe kaseweredwe kapereka kale chiyembekezo kuti timu ilibwino.
Iye amayankhula patsogolo pa masewero omwe akumane ndi Moyale Barracks loweruka masana ndipo wati timu yake iyesetsa kuti ipeze chipambano pa masewerowa.
"Akhala masewero ovuta chifukwa Moyale ndi timu yabwino ilinso ndi mphunzitsi wodziwa koma ifeyo takonzeka bwino, timu ikusewera bwino koma kuti tipeze zigoli zikuvuta," iye anatero.
Akidu anati timu yawo yakonza katchingidwe kumbuyo Komanso kuti azimwetsa zigoli zomwe zitawathandize kuti azichita bwino.
Timuyi ili pa nambala 14 pomwe ili ndi point imodzi pa masewero atatu omwe yasewera mu ligi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores