"Tapezana ndi matimu ovuta okha okha" - Fazili
Mphunzitsi watimu ya Scorchers, Lovemore Fazilo, wati akuyembekezera masewero ovuta okha okha ku mpikisano wa chaka chino wa COSAFA Womens Championship poti atola matimu abwino okhaokha.
Iye amayankhula atatha mayere omwe timuyi yaikidwa mu gulu loyamba momwe muli South Africa, Angola komanso Lesotho.
Iye wati mayerewa wawalandira bwino ndipo akonzekera mokwanira kuti akachite bwino.
"South Africa tinayimenya COSAFA yathayo titakumana nde tikonzekera bwino kuti tidzayigonjetse nde tidzayambira pomwe tinalekera," anatero Fazili.
Mpikisanowu uyamba pa 18 February mpaka pa 3 March 2026 ndipo Malawi ikuyang'ana zopambana chikho chawo chachiwiri cha mpikisanowu.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores