"Timu yathu yasinthika ndipo tipanga zinthu" - Nyambose
Mphunzitsi watimu ya Songwe Border United, Christopher Nyambose, wati timu yake tsopano yasinthika kwambiri pomwe ikusewerano zampira ndipo akukhulupilira kuti achita zinthu mu masewero omwe atsala nawo mu ligi.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 1-3 ndi timu ya FCB Nyasa Big Bullets mmasewero omwe anayamba kugoletsa kudzera mwa Kelvin Nyondo Koma Babatunde Adepoju anamwetsa ziwiri ndi kuthandiziranso cha Chikumbutso Salima ku mbali ya Bullets.
Iye wayamikira osewera ake kuti tsopano akumenya bwino ndipo mmasewero akudzawa akhale akuchita bwino.
"Tili ndi timu yosinthika kwambiri yomwe yaonetsa kuti ilibwino kusiyana ndi momwe inalili mchigawo choyamba nde tipanga zinthu mmasewero atsalawa." Anatero Nyambose.
Kugonjaku kunali kwachikhumi ndi kasanu pa masewero omwe yasewera mu ligi pomwe yangokwanitsa kufananitsa mphamvu kawiri kokha.
Iwo ali ndi mapointsi awiri pa masewero 17 kupezeka pansi penipeni pa ligi ya TNM.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores