"Pano tadzuka ndipo sitituluka" - Chirambo
Mphunzitsi watimu ya Mzuzu City Hammers, Elias Chirambo, wati timu yake tsopano yadzuka ndipo situluka mu ligi pomwe tsopano anyamata ake agwira mseu tsopano.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 1-2 ndi timu ya Ekhaya FC pa bwalo la Kamuzu ndipo wati timu yake inapita ndi mtima onse kufunitsitsa kupeza chipambano ndipo zatheka.
"Anyamata asewera bwino kwambiri kuonetsa kuti azitolera zomwe zikuonetsa kuti tayambapo ndipo kuti sitituluka mu ligi." Anatero Chirambo.
Iye anatinso kumapeto kwa masewerowa Oyimbira anafuna kukhala ku mbali ya Ekhaya poti inali pakhomo Koma mwa mwayi kuti timuyi inachilimika mpaka kupambana.
Chipambanochi chatengera timuyi kufika pa mapointsi okwana 11 pa masewero 16 omwe asewera pomwe apambana masewero atatu, kulepherana awiri ndi kugonja ka khumi ndi kamodzi.
📸 MH photography
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores