"Tiyesetsa kuti titengeko chikho cha FDH" - Mpinganjira
Mphunzitsi watimu ya Mighty Wanderers, Bob Mpinganjira, wati sizimakongola zoti timu yake simapezekapo pa ndandanda wa matimu omwe anatengako chikho cha FDH Bank ndipo alimbikira kuti chaka chino achitengeko.
Iye amayankhula atatha masewero omwe apambana 3-1 kuti afike mu ndime ya matimu 16 a chikhochi pomwe Isaac Kaliati, Blessings Singini ndi Felix Zulu anamwetsera timuyi.
Iye anati ndi wokondwa kamba koti anapeza chipambanochi ndipo alimbikirabe kuti mwina achite bwino mu ligiyi.
"Sitinapambaneko chikhochi ndiye tiyesetsa kulimbikira kuti mwina tichitengeko poti sizimakhala bwino kuti timu ngati Wanderers simapezeka pa matimu omwe anatengako chikhochi nde tilimbikira kuti tipambane." Anatero Mpinganjira.
Iye watinso akudziwa kuti masewero a mpikisanowu amakhala ovuta poti timu iliyonse imafunako itapambana komabe achilimike kuti achite bwino.
Wanderers idzakumana ndi owina pakati pa Mzuzu City Hammers ndi Baka City.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores