"Sindinakhutire, ndimafuna kupambana" - Mwansa
Mphunzitsi watimu ya Moyale Barracks, Prichard Mwansa, wati siwokhutira ndi kupeza point imodzi pa masewero awo ndi Mighty Wanderers poti amafuna apheretu masewero kamba koti ataya mapointsi mmasewero ochuluka.
Iye amayankhula atatha masewero omwe alepherana 1-1 ndi Wanderers pa bwalo la Rumphi komabe anayamikira osewera ake Kamba kosewera bwino makamaka mchigawo chachiwiri.
"Sindinakhutitsidwe ndi zotsatirazi chifukwa timayenera kupambana Kamba koti tataya mapointsi ochuluka mmasewero apitawa Koma sizinatheke, tiwayamikire osewera asewera bwino pomwe anachinyitsa Koma anayesetsa mpaka tinakwanitsa kubwenza chigolicho." Anatero Mwansa.
Iye watinso timu yawo ikuyenda mwa pendapenda mu ligiyi Koma akuona mavutowa ndipo akapumira Chigawo choyamba ayesetsa kuti adzachite bwino mchigawo chachiwiri.
Timuyi ili pa nambala 12 ndi mapointsi okwana 15 itapambana katatu, kufanana mphamvu kasanu ndi kamodzi (6) ndi kugonja kanayi.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores