Moyale yafa katatu kotsogozana
Zinthu sizikuyenda kutimu ya Moyale Barracks yomwe inali imodzi mwa matimu osagonja mu ligi pomwe yagonja katatu kotsogozana mu ligi chiyambireni kugonja kwawo koyamba.
Timuyi yagonjanso ndi Creck Sporting Club 1-0 pa bwalo la Aubrey Dimba pomwe kuchokera kogonja ndi Mzuzu City Hammers komanso FCB Nyasa Big Bullets zomwe zachititsa kuti atsike mu ligi.
Mphunzitsi watimuyi Prichard Mwansa wavomera kuti zinthu sizili bwino kutimu yake ndipo akuyenera kukonza cholinga ayambirenso kuchita bwino.
"Tikuchoka kogonja mmasewero awiri apanso tagonja nde zinthu sizili bwino. Timu ilibwino ndipo ikusewera bwino koma zotsatira zikuvuta nde tikufunika tikonze kuti ziyambe kuyenda." Anatero Mwansa.
Timuyi inali ndi osewera atatu okha panja pa masewerowa ndipo Iye wati ena ali ndi ma kadi ochuluka pomwe ena ndi ovulala.
Moyale ili pa nambala 9 mu ligi pomwe yatolera ma points 13 pa masewero khumi omwe yasewera ndipo yapambana katatu kufanana mphamvu kanayi kugonja
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores