"ZABWINOBWINO TIZISEWERA MPAKA KUMAPETO" - MWAKHWAWA
Mphunzitsi watimu ya Baka City, Victor Mwakhwawa, wati palibe chimene chaonongekapo pomwe timu yake isewere masewero omwe ali nawo mpaka kumaliza mu ligi ya TNM.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 2-1 ndi timu ya MAFCO lamulungu pa bwalo la Chitowe ndipo wati timu yake inasewera mwapamwamba koma inangovutika kuti pagolo pawo sipanali bwino.
Iye wati timu yake ipitilizabe kusewera mpaka pamapeto koma wati khalidwe ndi limene limavuta kwambiri kutimuyi kupangitsa kuti aziyenda ndi osewera ochepa pomwe panja pawo panali osewera awiri okha.
Timuyi ikadali pansi penipeni pa ligi pomwe ili ndi mapointsi okwana asanu ndi atatu (8) pa masewero 24 omwe yasewera mu ligi ya TNM.
Wolemba: Hastings Wadza Kasonga Jr
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores