"MASEWERO AKADALIPO TIKONZA MAVUTO ONSE" - YASIN
Mphunzitsi watimu ya Bangwe All Stars, Rodgers Yasin, wati timu yake ikhalebe ikukonza mavuto awo omwe akudutsamo kutimuyi ndipo mwayi ulipo otsala mu ligi poti masewero akadalipo ambiri.
Iye amayankhula atatha masewero omwe agonja 0-1 ndi timu ya Bangwe All Stars ndipo wati timu yake inapeza mipata yochuluka yomwe akanika kugwiritsa ntchito.
"Anali masewero ophweka kwambiri, mmene tinalili ndi mmene iwonso [a FOMO] analili, mimwayi tinali nawo ndithu kuti tikanatha kuchita bwino koma ukamaphonya mipata umalangika chotere." Anatero Yasin.
Timu ya Bangwe All Stars ili pa nambala yachikhumi ndi chisanu (15) pomwe ili ndi mapointsi okwana 12 pa masewero 18 omwe yasewera.
📷: Bangwe AS media
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores