"MTETEMERA AKADALI MPHUNZITSI WA CRECK" - SELEMANI
Wapampando wa timu ya Creck Sporting Club, Muhammad Selemani, wati Macdonald Mtetemera akadali mphunzitsi watimuyi pomwe akadali mkati mounikirabe mmene anachitira pomwe ankagwira ntchito.
Iye amayankhula atafunsira ndi Hastings Kasonga pa chifukwa chimene sananenerebe za tsogolo lake kutimuyi ndipo wati akuluakulu anali asanakumane koma posachedwa anene chitsogolo chake.
"NGINDE ndi mphunzitsi wathu kungoti anangoyimitsidwa kuti tiunikire mmene anachitira nthawi yomwe amagwira ntchito nde zachedwerapo chifukwa ena mwa akuluakulu anatangwanika koma tsopano takumana, chitsogolo tinena koma ndi mphunzitsi wathube timayankhulana ndipo amabwera." Anatero Selemani.
Iye wachenjeza matimu kuti azunzika mchigawo chachiwiri ndipo itayambe ndi Baka City loweruka likudzali pomwe akhale akukumana mu ligi.
Timuyi ili pa nambala yachisanu ndi chimodzi (6) pomwe ili ndi mapointsi 23 pa masewero 15 omwe yasewera.
Login with Facebook to post predictions, updates & live scores